Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nahumu 3:14-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Udzitungiretu madzi a nthawi yokumangira misasa, limbikitsa malinga ako, lowa kuthope, ponda dothi, limbitsa ng'anjo yanjerwa.

15. Pomwepo moto udzatha iwe; lupanga lidzakuononga; lidzatha iwe ngati cirimamine; udzicurukitse ngati cirimamine, udzicurukitse ngati dzombe.

16. Wacurukitsa amalonda ako koposa nyenyezi za kuthambo; cirimamine anyambita, nauluka, nathawa.

17. Obvala korona ako akunga dzombe, ndi akazembe, ndi akazembe ako ngati ziwalamsatsi zakutera m'macinga tsiku lacisanu, koma likafundukula dzuwa ziuluka nizithawa, ndi kumene zinakhalako sikudziwikanso.

18. Abusa ako aodzera, mfumu ya ku Asuri; omveka ako apumula; anthu ako amwazika pamapiri, ndipo palibe wakuwasonkhanitsa.

19. Palibe cakulunzitsa kutyoka kwako; bala lako liwawa; onse akumva mbiri yako akuombera manja; pakuti ndaniyo kuipa kwako sikunampitapitabe?

Werengani mutu wathunthu Nahumu 3