Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nahumu 3:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsoka mudzi wa mwazi! udzala nao mabodza ndi zacifwamba; zacifwamba sizidukiza.

2. Kumveka kwa cikoti, ndi mkokomo wa kuyenda kwa njinga za magareta; ndi kaphata kaphata wa akavalo, ndi gwegwegwe wa magareta;

3. munthu wokwera pa kavalo, ndi lupanga lonyezimira, ndi mkondo wong'anipa; ndi aunyinji ophedwa, ndi cimulu ca mitembo, palibe kutha zitanda; angokhumudwa ndi zitanda;

4. cifukwa ca ciwerewere cocuruka ca waciwerewere wokongola, ndiye mkaziyo mwini nyanga, wakugulitsa amitundu mwa ciwerewere cace, ndi mabanja mwa nyanga zace.

5. Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndidzaphimba nkhope yako ndi nsaru yako yoyesa mthendene; ndipo ndidzaonetsa amitundu umarisece wako, ndi maufumu manyazi ako.

6. Ndipo ndidzakuponyera zonyansa, ndi kukucititsa manyazi, ndi kukuika copenyapo,

7. Ndipo kudzali kuti onse akupenyerera iwe adzakuthawa, nadzati, Nineve wapasuka, adzamlira maliro ndani? ndidzakufunira kuti akukutonthoza?

8. Kodi uli wabwino woposa No-Amoni, wokhala pakati pa mitsinje wozingidwa ndi madzi; amene chemba lace ndilo nyanja, ndi linga lace ndilo nyanja?

9. Kusi ndi Aigupto ndiwo mphamvu yace, ndiyo yosatha, Puti ndi Lubimu ndiwo akukuthandiza.

10. Koma iye anatengedwa, analowa ndende; ana ace a makanda anaphwanyika polekeza pace pa miseu yace yonse; ndi pa omveka ace anacita maere, ndi akulu ace onse anamangidwa maunyolo.

11. Iwenso udzaledzera, udzabisala; iwenso udzafunanso polimbikira cifukwa ca mdani.

12. Malinga ako onse adzanga mikuyu ndi nkhuyu zoyamba kupsa; akaigwedeza zingokugwa m'kamwa mwa wakudya.

13. Taona, anthuako m'kati mwako akunga akazi; zipata za dziko lako zatsegulidwira adani ako papakuru; moto watha mipingiridzo yako.

Werengani mutu wathunthu Nahumu 3