Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nahumu 2:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Wophwanyayo wakwera pamaso pako; sunga linga, yang'anira panjira, limbitsa m'cuuno mwako, limbikitsatu mphamvu yako.

2. Pakuti Yehova abwezeranso ukulu wace wa Yakobo ngati ukulu wace wa Israyeli; pakuti okhuthula anawakhuthula, naipsa nthambi zace za mpesa.

3. Zikopa za amphamvu ace zasanduka zofiira, ngwazi zibvala mlangali; magareta anyezimira ndi citsulo tsiku la kukonzera kwace, ndi mikondo itinthidwa.

4. Magareta acita mkokomo m'miseu, akankhana m'makwalala; maonekedwe ao akunga miuni, athamanga ngati mphezi.

5. Akumbukila omveka ace; akhumudwa m'kupita kwao, afulumira ku linga lace, ndi cocinjiriza cakonzeka.

6. Pa zipata za mitsinje patseguka, ndi cinyumba casungunuka.

7. Catsimikizika, abvulidwa, atengedwa, adzakazi ace alira ngati mau a nkhunda, nadziguguda pacifuwa pao.

8. Koma Nineve wakhala ciyambire cace ngati thamanda lamadzi; koma athawa. Imani, Imani! ati, koma palibe woceuka.

9. Funkhani siliva, funkhani golidi; pakuti palibe kutha kwace kwa zosungikazo, kwa cuma ca zipangizo zofunika ziri zonse.

10. Ndiye mopanda kanthu mwacemo ndi mwacabe, ndi wopasuka; ndi mtima usungunuka, ndi maondo aombana, ndi m'zuuno zonse muwawa, ndi nkhope zao zatumbuluka.

Werengani mutu wathunthu Nahumu 2