Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nahumu 1:12-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Atero Yehova: Angakhale iwo ali ndi mphamvu yokwanira, nacuruka momwemo, koma momwemonso adzasalikidwa, ndipo iye adzapitiratu. Cinkana ndakuzunza iwe, sindidzakuzunzanso.

13. Koma tsopano ndidzatyola ndi kukucotsera goli lace, ndipo ndidzadula zomangira zako.

14. Ndipo Yehova walamulira za iwe kuti asabzalidwenso ena a dzina lako; m'nyumba ya milungu yako ndidzacotsa fano losema ndi fano loyenga; ndidzakukonzerapo manda, pakuti iwe ndiwe wopepuka.

15. Taonani pamapiri mapazi a iye wakulalikira uthenga wabwino, wakubukitsa mtendere! cita madyerero ako, Yuda, kwaniritsa zowinda zako; pakuti wopanda paceyo sadzapitanso mwa iwe; iye waonongeka konse.

Werengani mutu wathunthu Nahumu 1