1. Pakuti zonsezi ndinazisunga mumtima ndikalondoletu zonsezi; kuti olungama ndi anzeru ndi nchito zao ali m'manja a Mulungu; ngakhale kukonda ngakhale kudana anthu sadziwa; zonse ziri m'tsogolo mwao.
2. Zonse zigwera onse cimodzimodzi; kanthu kamodzi kangogwera wolungama ndi woipa; ngakhale wabwino ndi woyera ndi wodetsedwa: ngakhale wopereka nsembe ndi wosapereka konse; wabwino alingana ndi wocimwa; wolumbira ndi woopa lumbiro.