Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 8:3-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Usakangaze kumcokera; usaumirire kanthu koipa; pakuti iyeyo amacita comwe cimkonda.

4. Pakuti mau a mfumu ali ndi mphamvu; ndipo ndani anganene kwa iye, Kodi ucita ciani?

5. Wosunga cilamulo sadzadziwa kanthu koipa; ndipo mtima wa munthu wanzeru udziwa nyengo ndi maweruzo;

6. pakuti kanthu kali konse kali ndi nthawi yace ndi ciweruzo cace; popeza zoipa za munthu zimcurukira;

7. pakuti sadziwa cimene cidzakhala; pakuti ndani angamuuze nthawi yakuti cidzacitidwa?

8. Kulibe munthu ali ndi mphamvu yolamulira mzimu ndi yakutsekereza mzimu; ngakhale mphamvu tsiku la imfa; munkhondo umo mulibe kumasuka; udio sudzapulumutsa akuzolowerana nao.

9. Zonsezi ndaziona ndi kuyang'anitsa mtima wanga nchito zonse zicitidwa pansi pano; nthawi yakuti wina apweteka mnzace pomlamulira.

10. Ndipo ndinaona oipa alikuikidwa m'manda ndi kupita; ndipo omwe anacita zolungama anacokera ku malo opatulika a ku mudzi nawaiwala; icinso ndi cabe.

11. Popeza sambwezera coipa cace posacedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kucita zoipa.

12. Angakhale wocimwa acita zoipa zambirimbiri, masiku ace ndi kucuruka, koma ndidziwitsadi kuti omwe aopa Mulungu naopa pamaso pace adzapeza bwino;

13. koma woipa sadzapeza bwino ngakhale kutanimphitsa masiku ace ngati mthunzi; cifukwa saopa pamaso pa Mulungu.

14. Pali cinthu cacabe cimacitidwa pansi pano; cakuti alipo olungama amene aona zomwe ziyenera nchito za oipa, ndipo alipo oipa amene aona zomwe ziyenera nchito za olungama, Ndinati, Icinso ndi cabe.

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 8