Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 7:22-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. pakuti kawiri kawiritu mtima wako udziwa kuti nawenso unatemberera ena.

23. Ndayesa zonsezi ndi nzeru; ndinati, Ndidzakhala wanzeru, koma inanditarikira.

24. Cakutari ndi cakuyadi adzacipeza ndani?

25. Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udio ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;

26. ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wace ukunga maukonde, manja ace ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wocimwa adzagwidwa naye.

27. Taonani, ici ndacipeza, ati Mlalikiyo, m'kuphatikiza cinthu cina ndi cinzace, ndikazindikire malongosoledwe ao;

28. comwe moyo wanga ucifuna cifunire, koma osacipezai ndi ici, mwamuna mmodzi mwa cikwi ndinampezadi, koma mkazitu mwa onsewo sindinampeza.

29. Taonani, ici cokha ndacipeza kuti Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundu mitundu.

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 7