20. Pakuti kulibe wolungama pansi pano amene acita zabwino osacimwa.
21. Mau onsetu onenedwa usawalabadire; kuti usamve kapolo wako alikukutemberera;
22. pakuti kawiri kawiritu mtima wako udziwa kuti nawenso unatemberera ena.
23. Ndayesa zonsezi ndi nzeru; ndinati, Ndidzakhala wanzeru, koma inanditarikira.
24. Cakutari ndi cakuyadi adzacipeza ndani?
25. Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udio ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;
26. ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wace ukunga maukonde, manja ace ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wocimwa adzagwidwa naye.