Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 5:13-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Pali coipa cobvuta ndaciona kunja kuno, ndico, cuma cirikupweteka eni ace pocikundika;

14. koma cumaco cionongeka pomgwera tsoka; ndipo akabala mwana, m'dzanja lace mulibe kanthu.

15. Monga anaturuka m'mimba ya amace, adzabweranso kupita wamarisece, monga anadza osatenga kanthu pa nchito zace, kakunyamula m'dzanja lace.

16. Icinso ndi coipa cowawa, cakuti adzangopita monse monga anadza; ndipo wodzisautsa cabe adzaona phindu lanji?

17. Inde masiku ace onse amadya mumdima, nizimcurukira cisoni ndi nthenda ndi mkwiyo.

18. Taonani, comwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi nchito zace zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wace umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lace limeneli.

19. Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa cuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lace ndi kukondwera ndi nchito zace; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu.

20. Pakuti sadzakumbukira masiku a moyo wace kwambiri; cifukwa Mulungu ambvomereza m'cimwemwe ca mtima wace.

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 5