1. Samalira phazi lako popita ku nyumba ya Mulungu; pakuti kuyandikira kumvera kupambana kupereka nsembe za zitsiru; pakuti sizizindikira kuti zirikucimwa.
2. Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; cifukwa cace mau ako akhale owerengeka.
3. Pakuti loto lafika mwakucuruka nchito; ndipo mau a citsiru mwakucuruka maneno.
4. Utawinda ciwindo kwa Mulungu, usacedwe kucicita; pakuti sakondwera ndi zitsiru; cita comwe unaciwindaco.
5. Kusawinda kupambana kuwinda osacita,
6. Usalole m'kamwa mwako mucimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako cifukwa ninji, naononge nchito ya manja ako?
7. Pakuti monga mu unyinji wa maloto muli zacabe motero mocuruka mau; koma dziopa Mulungu.
8. Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kucotsa cilungamo ndi ciweruzo mwaciwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkuru wopambana asamalira; ndipo alipo akuru ena oposa amenewo.
9. Phindutu la dziko lipindulira onse; ngakhale mfumu munda umthandiza.