Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 4:7-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Pamenepo ndinabwera ndi kupenyera zacabe kunja kuno.

8. Pali mmodzi palibe waciwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma nchito yace yonse iribe citsiriziro, ngakhale diso lace silikhuta cuma. Samati, Ndigwira nchito ndi kumana moyo wanga zabwino cifukwa ca yani? Icinso ndi cabe, inde, bvuto lalikuru.

9. Awiri aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphotho yabwino m'nchito zao.

10. Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzace; koma tsoka wakugwa wopanda womnyamutsa.

11. Ndiponso awiri akagona limodzi afunditsana; koma mmodzi pa yekha kodi adzafunditsidwa bwanji?

12. Ndipo wina akamlaka mmodziyo, awiri adzacirimika; ndipo cingwe ca nkhosi zitatu siciduka msanga.

13. Mnyamata wosauka ndi wanzeru apambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene sifunanso kulangidwa mwambo.

14. Pakuti aturuka m'nyumba yandende kulowa ufumu; komanso yemwe abadwa m'dziko lace asauka.

15. Ndinapenyera anthu onse amoyo akuyenda kunja kuno, kuti anali ndi mwana, waciwiri, amene adzalowa m'malo mwace.

16. Anthu onse sawerengeka, ngakhale onsewo anawalamulira; koma amene akudza m'mbuyo sadzakondwera naye. Icinso ndi cabe nicisautsa mtima.

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 4