Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 2:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo ciri conse maso anga anacifuna sindinawamana; sindinakaniza mtima wanga cimwemwe ciri conse pakuti mtima wanga unakondwera ndi nchito zanga zonse; gawo langa la m'nchito zanga zonse ndi limeneli.

11. Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi nchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zacabecabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.

12. Ndipo ndinatembenuka kukayang'ana nzeru ndi misala ndi utsiru; pakuti yemwe angotsata mfumu angacite ciani? Si comwe cinacitidwa kale.

13. Pamenepo ndinazindikira kuti nzeru ipambana utsiru kwambiri, monga kuunika kupambana mdima.

14. Wanzeru maso ace ali m'mutu wace, koma citsiru ciyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti comwe ciwagwera onsewo ndi cimodzi.

15. Pamenepo ndinati mumtima mwanga, Comwe cigwera citsiru nanenso cindigwera; nanga bwanji ndinapambana kukhala wanzeru? Pamenepo ndinati mumtima mwanga kuti icinso ndi cabe.

16. Pakuti wanzerusaposa citsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m'tsogolomo, Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati citsirutu.

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 2