Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 11:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ponya zakudya zako pamadzi; udzazipeza popita masiku ambiri.

2. Gawira asanu ndi awiri ngakhale asanu ndi atatu; pakuti sudziwa coipa canji cidzaoneka pansi pano.

3. Mitambo ikadzala mvula, itsanulira pansi; mtengo ukagwa kumwela pena kumpoto, pomwe unagwa mtengowo udzakhala pomwepo.

4. Woyang'ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.

5. Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m'mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa nchito za Mulungu amene acita zonse.

6. Mamawa fesa mbeu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino.

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 11