1. Nzeru yamanga nyumba yace,Yasema zoimiritsa zace zisanu ndi ziwiri;
2. Yaphera nyama yace, nisanganiza vinyo wace,Nilongosolanso pa gome lace.
3. Yatuma anamwali ace, iitanaPa misanje ya m'mudzi.
4. Wacibwana yense apambukire kuno;Iti kwa yense wosowa nzeru,
5. Tiyeni, idyani cakudya canga;Nimumwe vinyo wanga ndamsanganiza.
6. Lekani, acibwana inu, nimukhale ndi moyo;Nimuyende m'njira ya nzeru.
7. Woweruza munthu wonyoza adzicititsa yekha manyazi;Yemwe adzudzula wocimwa angodetsa mbiri yace yace.