Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 8:27-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Pamene anakhazika mlengalenga ndinali pompo;Pamene analemba pazozama kwete kwete;

28. Polimbitsa Iye thambo la kumwamba,Pokula akasupe a zozama.

29. Poikira nyanja malire ace,Kuti madzi asapitirire pa lamulo lace;Polemba maziko a dziko,

30. Ndinali pa mbali pace ngati mmisiri;Ndinamsekeretsa tsiku ndi tsiku,Ndi kukondwera pamaso pace nthawi zonse;

31. Ndi kukondwera ndi dziko lace lokhalamo anthu,Ndi kusekerera ndi ana a anthu.

32. Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine,Ngodala akusunga njira zanga.

33. Imvani mwambo, mukhale anzeru osaukana.

34. Ngwodala amene andimvera, nadikira pa zitseko zanga tsiku ndi tsiku,Ndi kulinda pa mphuthu za makoma anga;

35. Pakuti wondipeza ine apeza moyo;Yehova adzamkomera mnma.

36. Koma wondicimwira apweteka moyo wace;Onse akundida ine akonda imfa.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 8