Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 27:3-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Mwala ulemera, mcenga ndiwo katundu;Koma mkwiyo wa citsiru upambana kulemera kwace.

4. Kupweteka mtima nkwa nkhanza, mkwiyo usefuka;Koma ndani angalakike ndi nsanje?

5. Cidzudzulo comveka ciposa cikondi cobisika.

6. Kulasa kwa bwenzi kulikokhulupirika;Koma mdani apsompsona kawiri kawiri.

7. Mtima wokhuta upondereza cisa ca uci;Koma wakumva njala ayesa zowawa zonse zotsekemera.

8. Monga mbalame yosocera ku cisa cace,Momwemo munthu wosocera ku malo ace.

9. Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima,Ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu,

10. Mnzako, ndi mnzace wa atate wako, usawasiye;Usanke ku nyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako;Mnansi wapafupi aposa mbale wakutari.

11. Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga;Kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.

12. Wocenjera aona zoipa, nabisala;Koma acibwana angopitirira, nalipitsidwa.

13. Tenga maraya a woperekera mlendo cikole;Woperekera mkazi waciwerewere cikole umgwire mwini.

14. Yemwe adalitsa mnzace ndi mau akuru pouka mamawa,Anthu adzaciyesa cimeneco temberero.

15. Kudonthadontha tsiku lamvula,Ndi mkazi wolongolola ali amodzimodzi.

16. Wofuna kumletsayo afuna kuletsa mphepo;Dzanja lace lamanja lingogwira mafuta.

17. Citsulo cinola citsulo;Comweco munthu anola nkhope ya mnzace.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 27