Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 25:10-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Kuti wakumva angakutonze,Mbiri yako yoipa ndi kusacoka.

11. Mau oyenera a pa nthawi yaceAkunga zipatso zagolidi m'nsengwa zasiliva.

12. Monga phelele lagolidi ndi cipini cagolidi woyengeka,Momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.

13. Monga cisanu ca cipale cofewa pa nthawi ya masika,Momwemo mthenga wokhulupirika kwa amene anamtuma;Atsitsimutsa moyo wa ambuyace.

14. Monga mitambo ndi mphepo popanda mvula,Momwemo ndiye wodzikweza ndi zipatso zace monyenga.

15. Cipiriro cipembedza mkuru;Lilime lofatsa lityola pfupa,

16. Wapeza uci kodi? Idyapo wokwanira,Kuti ungakukole, nusanze.

17. Phazi lako lilowe m'nyumba ya mnzako kamodzi kamodzi;Kuti angatope nawe ndi kukuda.

18. Wocitira mnzace umboni wonamaNdiye cibonga, ndi lupanga, ndi mubvi wakuthwa.

19. Kukhulupirira munthu wa ciwembu tsiku latsokaKunga dzino lotyoka ndi phazi loguluka.

20. Monga wobvula maraya tsiku lamphepo,Ngakhale kuthira vinyo wosasa m'soda,Momwemo woyimbira nyimbo munthu wacisoni.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 25