16. Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi waciwerewere,Kwa mkazi wacilendo wosyasyalika ndi mau ace;
17. Wosiya bwenzi la ubwana wace,Naiwala cipangano ca Mulungu wace;
18. Nyumba yace itsikira kuimfa,Ndi mayendedwe ace kwa akufa;
19. Onse akunka kwa iye sabweranso,Safika ku njira za moyo;
20. Nzeru idzakuyendetsa m'njira ya anthu abwino,Kuti usunge mayendedwe a olungama.
21. Pakuti oongoka mtima adzakhala m'dziko,Angwiro nadzatsalamo.
22. Koma oipa adzalikhidwa m'dziko,Aciwembu adzazulidwamo.