Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 2:10-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pakuti nzeru idzalowa m'mtima mwako,Moyo wako udzakondwera ndi kudziwa,

11. Kulingalira kudzakudikira,Kuzindikira kudzakucinjiriza;

12. Kukupulumutsa ku njira yoipa,Kwa anthu onena zokhota;

13. Akusiya mayendedwe olungama,Akayende m'njira za mdima;

14. Omwe asangalala pocita zoipa,Nakondwera ndi zokhota zoipa;

15. Amene apotoza njira zao,Nakhotetsa mayendedwe ao;

16. Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi waciwerewere,Kwa mkazi wacilendo wosyasyalika ndi mau ace;

17. Wosiya bwenzi la ubwana wace,Naiwala cipangano ca Mulungu wace;

18. Nyumba yace itsikira kuimfa,Ndi mayendedwe ace kwa akufa;

19. Onse akunka kwa iye sabweranso,Safika ku njira za moyo;

20. Nzeru idzakuyendetsa m'njira ya anthu abwino,Kuti usunge mayendedwe a olungama.

21. Pakuti oongoka mtima adzakhala m'dziko,Angwiro nadzatsalamo.

22. Koma oipa adzalikhidwa m'dziko,Aciwembu adzazulidwamo.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 2