13. Wobwezera mau asanamvetse apusa,Nadzicititsa manyazi.
14. Mtima wa munthu umlimbitsa alikudwala;Koma ndani angatukule mtima wosweka?
15. Mtima wa wozindikira umaphunzira;Khutu la anzeru lifunitsa kudziwa.
16. Mtulo wa munthu umtsegulira njira,Numfikitsa pamaso pa akuru.
17. Woyamba kudzinenera ayang'anika wolungama;Koma mnzace afika namuululitsa zace zonse.
18. Ula uletsa makangano,Nulekanitsa amphamvu.
19. Kupembedza mbale utamcimwira nkobvuta,Kulanda mudzi wolimba nkosabvuta;Makangano akunga mipiringidzo ya linga.
20. Mimba ya munthu idzakhuta zipatso za m'kamwa mwace;Iye nadzakhuta phindu la milomo yace.
21. Lilime liri ndi mphamvu pa imfa ndi moyo;Wolikonda adzadya zipatso zace.
22. Wopeza mkazi apeza cinthu cabwino;Yehova amkomera mtima.
23. Wosauka amadandaulira;Koma wolemera ayankha mwaukali.