1. Wopanduka afunafuna niro cace,Nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.
2. Wopusa sakondwera ndi kuzindikira;Koma kungobvumbulutsa za m'mtima mwace.
3. Pakudza wamphulupulu padzanso kunyoza;Manyazi natsagana ndi citonzo.
4. Mau a m'kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya;Kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wodzala.