25. Yehova adzapasula nyumba ya wonyada;Koma adzalembera mkazi wamasiye malire ace,
26. Ziwembu zoipa zinyansa Yehova;Koma oyera mtima alankhula mau okondweretsa.
27. Wopindula monyenga abvuta nyumba yace;Koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo.
28. Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe;Koma m'kamwa mwa ocimwa mutsanulira zoipa.
29. Yehova atarikira oipa;Koma pemphero la olungama alimvera.
30. Kuunika kwa maso kukondweretsa mtima;Ndipo pomveka zabwino mafupa amatenga uwisi.
31. Khutu lomvera cidzudzulo ca moyoLidzakhalabe mwa anzeru.
32. Wokana mwambo apeputsa moyo wace;Koma wosamalira cidzudzulo amatenga nzeru.