6. Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza;Koma wozindikira saona bvuto m'kuphunzira.
7. Pita pamaso pa munthu wopusa,Sudzazindikira milomo yakudziwa.
8. Nzeru ya wocenjera ndiyo yakuti azindikire njira yace;Koma utsiru wa opusa ndiwo cinyengo.
9. Zitsiru zinyoza kuparamula;Koma mwa oongoka mtima muli ciyanjano.
10. Mtima udziwa kuwawa kwace kwace;Mlendo sadudukira ndi cimwemwe cace.
11. Nyumba ya oipa idzapasuka;Koma hema wa oongoka mtima adzakula.
12. Iripo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka;Koma matsiriziro ace ndi njira za imfa.
13. Ngakhale m'kuseka mtima uwawa;Ndipo matsiriziro a ciphwete ndi cisoni.
14. Wobwerera m'mbuyo m'mtima adzakhuta njira zace;Koma munthu wabwino adzakhuta za mwa iye yekha.
15. Wacibwana akhulupirira mau onse;Koma wocenjera asamalira mayendedwe ace.
16. Wanzeru amaopa nasiya zoipa;Koma wopusa amanyada osatekeseka.
17. Wokangaza kukwiya adzacita utsiru;Ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa.
18. Acibwana amalandira colowa ca utsiru;Koma ocenjera amabvala nzeru ngati korona.
19. Oipa amagwadira abwino,Ndi ocimwa pa makomo a olungama.
20. Waumphawi adedwa ndi anzace omwe;Koma akukonda wolemera acuruka.
21. Wonyoza anzace acimwa;Koma wocitira osauka cifundo adala.