Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 14:22-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Kodi oganizira zoipa sasocera?Koma akuganizira zabwino adzalandira cifundo ndi ntheradi.

23. M'nchito zonse muli phindu;Koma kulankhula-lankhula kungopatsa umphawi.

24. Korona wa anzeru ndi cuma cao;Utsiru wa opusa ndiwo utsiru.

25. Mboni yoona imalanditsa miyoyo;Koma wolankhula zonama angonyenga.

26. Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba;Ndipo ana ace adzakhala ndi pothawirapo.

27. Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo,Kupatutsa ku misampha ya imfa.

28. Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu;Koma popanda anthu kalonga aonongeka.

29. Wosakwiya msanga apambana kumvetsa;Koma wansontho akuza utsiru.

30. Mtima wabwino ndi moyo wa thupi;Koma nsanje ibvunditsa mafupa.

31. Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wace;Koma wocitira wosauka cifundo amlemekeza.

32. Wocimwa adzakankhidwa m'kuipa kwace;Koma wolungama akhulupirirabe pomwalira,

33. Nzeru ikhalabe m'mtima wa wozindikira,Nidziwika pakati pa opusa.

34. Cilungamo cikuza mtundu wa anthu;Koma cimo licititsa pfuko manyazi.

35. Mfumu ikomera mtima kapolo wocita mwanzeru;Koma idzakwiyira wocititsa manyazi.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 14