21. Wonyoza anzace acimwa;Koma wocitira osauka cifundo adala.
22. Kodi oganizira zoipa sasocera?Koma akuganizira zabwino adzalandira cifundo ndi ntheradi.
23. M'nchito zonse muli phindu;Koma kulankhula-lankhula kungopatsa umphawi.
24. Korona wa anzeru ndi cuma cao;Utsiru wa opusa ndiwo utsiru.
25. Mboni yoona imalanditsa miyoyo;Koma wolankhula zonama angonyenga.
26. Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba;Ndipo ana ace adzakhala ndi pothawirapo.
27. Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo,Kupatutsa ku misampha ya imfa.
28. Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu;Koma popanda anthu kalonga aonongeka.
29. Wosakwiya msanga apambana kumvetsa;Koma wansontho akuza utsiru.
30. Mtima wabwino ndi moyo wa thupi;Koma nsanje ibvunditsa mafupa.
31. Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wace;Koma wocitira wosauka cifundo amlemekeza.
32. Wocimwa adzakankhidwa m'kuipa kwace;Koma wolungama akhulupirirabe pomwalira,
33. Nzeru ikhalabe m'mtima wa wozindikira,Nidziwika pakati pa opusa.