Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 14:20-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Waumphawi adedwa ndi anzace omwe;Koma akukonda wolemera acuruka.

21. Wonyoza anzace acimwa;Koma wocitira osauka cifundo adala.

22. Kodi oganizira zoipa sasocera?Koma akuganizira zabwino adzalandira cifundo ndi ntheradi.

23. M'nchito zonse muli phindu;Koma kulankhula-lankhula kungopatsa umphawi.

24. Korona wa anzeru ndi cuma cao;Utsiru wa opusa ndiwo utsiru.

25. Mboni yoona imalanditsa miyoyo;Koma wolankhula zonama angonyenga.

26. Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba;Ndipo ana ace adzakhala ndi pothawirapo.

27. Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo,Kupatutsa ku misampha ya imfa.

28. Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu;Koma popanda anthu kalonga aonongeka.

29. Wosakwiya msanga apambana kumvetsa;Koma wansontho akuza utsiru.

30. Mtima wabwino ndi moyo wa thupi;Koma nsanje ibvunditsa mafupa.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 14