Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 14:17-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Wokangaza kukwiya adzacita utsiru;Ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa.

18. Acibwana amalandira colowa ca utsiru;Koma ocenjera amabvala nzeru ngati korona.

19. Oipa amagwadira abwino,Ndi ocimwa pa makomo a olungama.

20. Waumphawi adedwa ndi anzace omwe;Koma akukonda wolemera acuruka.

21. Wonyoza anzace acimwa;Koma wocitira osauka cifundo adala.

22. Kodi oganizira zoipa sasocera?Koma akuganizira zabwino adzalandira cifundo ndi ntheradi.

23. M'nchito zonse muli phindu;Koma kulankhula-lankhula kungopatsa umphawi.

24. Korona wa anzeru ndi cuma cao;Utsiru wa opusa ndiwo utsiru.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 14