11. Nyumba ya oipa idzapasuka;Koma hema wa oongoka mtima adzakula.
12. Iripo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka;Koma matsiriziro ace ndi njira za imfa.
13. Ngakhale m'kuseka mtima uwawa;Ndipo matsiriziro a ciphwete ndi cisoni.
14. Wobwerera m'mbuyo m'mtima adzakhuta njira zace;Koma munthu wabwino adzakhuta za mwa iye yekha.
15. Wacibwana akhulupirira mau onse;Koma wocenjera asamalira mayendedwe ace.
16. Wanzeru amaopa nasiya zoipa;Koma wopusa amanyada osatekeseka.
17. Wokangaza kukwiya adzacita utsiru;Ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa.
18. Acibwana amalandira colowa ca utsiru;Koma ocenjera amabvala nzeru ngati korona.
19. Oipa amagwadira abwino,Ndi ocimwa pa makomo a olungama.
20. Waumphawi adedwa ndi anzace omwe;Koma akukonda wolemera acuruka.
21. Wonyoza anzace acimwa;Koma wocitira osauka cifundo adala.
22. Kodi oganizira zoipa sasocera?Koma akuganizira zabwino adzalandira cifundo ndi ntheradi.
23. M'nchito zonse muli phindu;Koma kulankhula-lankhula kungopatsa umphawi.
24. Korona wa anzeru ndi cuma cao;Utsiru wa opusa ndiwo utsiru.
25. Mboni yoona imalanditsa miyoyo;Koma wolankhula zonama angonyenga.
26. Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba;Ndipo ana ace adzakhala ndi pothawirapo.
27. Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo,Kupatutsa ku misampha ya imfa.