Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 14:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mkazi yense wanzeru amanga banja lace;Koma wopusa alipasula ndi manja ace.

2. Woyenda moongoka mtima aopa Yehova;Koma wokhota m'njira yace amnyoza,

3. M'kamwa mwa citsiru muli ntyole ya kudzikuza;Koma milomo ya anzeru Idzawasunga.

4. Popanda zoweta modyera muti see;Koma mphamvu ya ng'ombe icurukitsa phindu.

5. Mboni yokhulupirika sidzanama;Koma mboni yonyenga imalankhula zonama.

6. Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza;Koma wozindikira saona bvuto m'kuphunzira.

7. Pita pamaso pa munthu wopusa,Sudzazindikira milomo yakudziwa.

8. Nzeru ya wocenjera ndiyo yakuti azindikire njira yace;Koma utsiru wa opusa ndiwo cinyengo.

9. Zitsiru zinyoza kuparamula;Koma mwa oongoka mtima muli ciyanjano.

10. Mtima udziwa kuwawa kwace kwace;Mlendo sadudukira ndi cimwemwe cace.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 14