7. Alipo wodziyesa wolemera, koma alibe kanthu;Alipo wodziyesa wosauka, koma ali ndi cuma cambiri.
8. Ciombolo ca moyo wa munthu ndico cuma cace;Koma wosauka samva cidzudzulo.
9. Kuunika kwa olungama kukondwa;Koma nyali ya oipa idzazima.
10. Kudzikuza kupikisanitsa;Koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.
11. Cuma colandiridwa mokangaza cidzacepa;Koma wokundika ndi dzanja adzaona zocuruka.
12. Ciyembekezo cozengereza cidwalitsa mtima;Koma pakufika cifuniroco ndico mtengo wa moyo.
13. Wonyoza mau adziononga yekha;Koma woopa malangizo adzalandira mphotho.
14. Malamulo a wanzeru ndiwo kasupe wa moyo,Apatutsa ku misampha ya imfa.
15. Nzeru yabwino ipatsa cisomo;Koma njira ya aciwembu iri makolokoto.