21. Zoipa zilondola ocimwa;Koma olungama adzalandira mphotho yabwino.
22. Wabwino asiyira zidzukulu zace colowa cabwino;Koma wocimwa angosungira wolungama cuma cace.
23. M'kulima kwa osauka muli zakudya zambiri;Koma zinazo zimaonongeka posowa ciweruzo.
24. Wolekereramwanace osammenya amuda;Koma womkonda amyambize kumlanga.
25. Wolungama adya nakhutitsa moyo wace;Koma mimba ya oipa idzasowa.