Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 13:18-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Wokana mwambo adzasauka nanyozedwa;Koma wolabadira cidzudzulo adzalemekezedwa.

19. Cifuniro cikondweretsa moyo citacitidwa;Koma kusiya zoipa kunyansa opusa,

20. Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru:Koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.

21. Zoipa zilondola ocimwa;Koma olungama adzalandira mphotho yabwino.

22. Wabwino asiyira zidzukulu zace colowa cabwino;Koma wocimwa angosungira wolungama cuma cace.

23. M'kulima kwa osauka muli zakudya zambiri;Koma zinazo zimaonongeka posowa ciweruzo.

24. Wolekereramwanace osammenya amuda;Koma womkonda amyambize kumlanga.

25. Wolungama adya nakhutitsa moyo wace;Koma mimba ya oipa idzasowa.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 13