21. Palibe bvuto lidzagwera wolungama;Koma amphulupulu adzadzazidwa ndi zoipa,
22. Milomo yonama inyansa Yehova;Koma ocita ntheradi amsekeretsa.
23. Munthu wanzeru abisa zomwe adziwa;Koma mtima wa opusa ulalikira utsiru.
24. Dzanja la akhama lidzalamulira;Koma wolesi adzakhala ngati kapolo,
25. Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu;Koma mau abwino aukondweretsa.
26. Wolungama atsogolera mnzace;Koma njira ya oipa iwasokeretsa.
27. Wolesi samaocha nyama yace anaigwira;Koma wolungama amalandira cuma copambana ca anthu.
28. M'khwalala la cilungamo muli moyo;M'njira ya mayendedwe ace mulibe imfa.