Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 12:12-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Woipa akhumba cokodwa ndi amphulupulu;Koma muzu wa olungama umabala zipatso.

13. M'kulakwa kwa milomo muli msampha woipa;Koma wolungama amaturuka m'mabvuto.

14. Munthu amakhuta zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwace;Zocita za manja ace zidzabwezedwa kwa iye.

15. Njira ya citsiru nlolungama pamaso pace pace;Koma wanzeru amamvera uphungu.

16. Mkwiyo wa citsiru udziwika posacedwa;Koma wanzeru amabisa manyazi.

17. Wolankhula ntheradi aonetsa cilungamo;Koma mboni yonama imanyenga.

18. Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga;Koma lilime la anzeru lilamitsa.

19. Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse;Koma lilime lonama likhala kamphindi.

20. Cinyengo ciri m'mitima ya oganizira zoipa;Koma aphungu a mtendere amakondwa.

21. Palibe bvuto lidzagwera wolungama;Koma amphulupulu adzadzazidwa ndi zoipa,

22. Milomo yonama inyansa Yehova;Koma ocita ntheradi amsekeretsa.

23. Munthu wanzeru abisa zomwe adziwa;Koma mtima wa opusa ulalikira utsiru.

24. Dzanja la akhama lidzalamulira;Koma wolesi adzakhala ngati kapolo,

25. Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu;Koma mau abwino aukondweretsa.

26. Wolungama atsogolera mnzace;Koma njira ya oipa iwasokeretsa.

27. Wolesi samaocha nyama yace anaigwira;Koma wolungama amalandira cuma copambana ca anthu.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 12