Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 12:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Wolungama asamalira moyo wa coweta cace;Koma cifundo ca oipa ndi nkhanza.

11. Zakudyazikwanira wolima minda yace;Koma wotsata anthu opanda pace asowa nzeru.

12. Woipa akhumba cokodwa ndi amphulupulu;Koma muzu wa olungama umabala zipatso.

13. M'kulakwa kwa milomo muli msampha woipa;Koma wolungama amaturuka m'mabvuto.

14. Munthu amakhuta zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwace;Zocita za manja ace zidzabwezedwa kwa iye.

15. Njira ya citsiru nlolungama pamaso pace pace;Koma wanzeru amamvera uphungu.

16. Mkwiyo wa citsiru udziwika posacedwa;Koma wanzeru amabisa manyazi.

17. Wolankhula ntheradi aonetsa cilungamo;Koma mboni yonama imanyenga.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 12