1. Wokonda mwambo akonda kudziwa;Koma wakuda cidzudzulo apulukira.
2. Yehova akomera mtima munthu wabwino;Koma munthu wa ziwembu amtsutsa,
3. Munthu sadzakhazikika ndi udio,Muzu wa olungama sudzasunthidwa.
4. Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wace;Koma wocititsa manyazi akunga cobvunditsa mafupa a mwamunayo.
5. Maganizo a olungama ndi ciweruzo;Koma uphungu wa oipa unyenga.
6. Mau a oipa abisalira mwazi;Koma m'kamwa mwa olungama muwalanditsa.
7. Oipa amagwa kuli zi;Koma banja la olungama limaimabe.
8. Munthu amatamandidwa monga mwa nzeru yace;Koma wokhota mtima adzanyozedwa.