9. Wonyoza Mulungu aononga mnzace ndi m'kamwa mwace;Koma olungama adzapulumuka pakudziwa,
10. Olungama akapeza bwino, mudzi usekera;Nupfuula pakuonongeka oipa.
11. Madalitso a olungama akuza mudzi;Koma m'kamwa mwa oipa muupasula.
12. Wopeputsa mnzace asowa nzeru;Koma wozindikira amatonthola.
13. Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi;Koma wokhulupirika mtima abisa mau.
14. Popanda upo wanzeru anthu amagwa;Koma pocuruka aphungu pali cipulumutso.
15. Woperekera mlendo cikole adzaphwetekwapo;Koma wakuda cikole akhala ndi mtendere.
16. Mkazi wodekha agwiritsa ulemu;Aukali nagwiritsa cuma.
17. Wacifundo acitira moyo wace zokoma;Koma wankhanza abvuta nyama yace.
18. Woipa alandira malipiro onyenga;Koma wofesa cilungamo aonadi mphotho,
19. Wolimbikira cilungamo alandira moyo;Koma wolondola zoipa adzipha yekha,
20. Okhota mtima anyansa Yehova;Koma angwiro m'njira zao amsekeretsa.