3. Kuongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera;Koma kukhota kwa aciwembu kudzawaononga.
4. Cuma sicithandiza tsiku la mkwiyo;Koma cilungamo cipulumutsa kuimfa.
5. Cilungamo ca wangwiro cimaongola njira yace;Koma woipa adzagwa ndi zoipa zace.
6. Cilungamo ca oongoka mtima cidzawapulumutsa;Koma aciwembu adzagwidwa ndi mphulupulu yao.
7. Pomwalira woipa cidikiro cace cionongeka;Ciyembekezo ca ucimo cionongeka.
8. Wolungama apulumuka kubvuto;Woipa nalowa m'malo mwace.
9. Wonyoza Mulungu aononga mnzace ndi m'kamwa mwace;Koma olungama adzapulumuka pakudziwa,
10. Olungama akapeza bwino, mudzi usekera;Nupfuula pakuonongeka oipa.