25. Mtima wa mataya udzalemera;Wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.
26. Womana tirigu anthu amtemberera;Koma madalitso adzakhala pamtu pa wogulitsa.
27. Wopwaira ubwino afunitsa cikondwerero;Koma zoipa zidzamfikira wozilondola.
28. Wokhulupmra cuma cace adzagwa;Koma olungama adzaphuka ngati tsamba.
29. Wobvuta banja lace adzalowa m'zomsautsa;Wopusa adzatumikira wanzeru.
30. Cipatso ca wolungama ndi mtengo wa moyo;Ndipo wokola mtima ali wanzeru.
31. Taonani, wolungama adzalandira mphotho kunja kuno;Koposa kotani woipa ndi wocimwa?