23. Cifuniro ca olungama cifikitsa zabwino zokha;Koma ciyembekezo ca oipa mkwiyo.
24. Alipo wogawira, nangolemerabe;Aliponso womana comwe ayenera kupatsa nangosauka.
25. Mtima wa mataya udzalemera;Wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.
26. Womana tirigu anthu amtemberera;Koma madalitso adzakhala pamtu pa wogulitsa.
27. Wopwaira ubwino afunitsa cikondwerero;Koma zoipa zidzamfikira wozilondola.
28. Wokhulupmra cuma cace adzagwa;Koma olungama adzaphuka ngati tsamba.
29. Wobvuta banja lace adzalowa m'zomsautsa;Wopusa adzatumikira wanzeru.
30. Cipatso ca wolungama ndi mtengo wa moyo;Ndipo wokola mtima ali wanzeru.