Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 1:6-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Kuzindikira mwambi ndi tanthauzo lace,Mau a anzeru, ndi zophiphiritsa zao.

7. Kuopa Yehova ndiko ciyambi ca kudziwa;Opusa anyoza nzeru ndi mwambo.

8. Mwananga, tamva mwambo wa atate wako,Ndi kusasiya cilangizo ca amako

9. Pakuti izi ndi korona wa cisomo pamtu pako,Ndi mkanda pakhosi pako.

10. Mwananga, akakukopa ocimwa usalole.

11. Akanena, Idza nafe, tibisalire mwazi,Tilalire osacimwa opanda cifukwa;

12. Tiwameze ali ndi moyo ngati manda,Ali amphumphu, ngati akutsikira kudzenje;

13. Tidzapeza cuma conse ca mtengo wace,Tidzadzaza nyumba zathu ndi zofunkha;

14. Udzacita nafe maere,Tonse tidzakhala ndi cibeti cimodzi;

15. Mwananga, usayende nao m'njira;Letsa phazi lako ku mayendedwe ao;

16. Pakuti mapazi ao athamangira zoipa,Afulumira kukhetsa mwazi.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 1