26. Inetu ndidzacitiraciphwete tsoka lanu,Ndidzatonyola pakudza mantha anu;
27. Pakudza mantha anu ngati mphepo yopasula,Ndi pofika tsoka lanu ngati kabvumvulu;Pakudza kwa inu bvuto ndi nsautso.
28. Pamenepo adzandiitana, koma sindidzabvomera;Adzandifunatu, osandipeza ai;
29. Cifukwa anada nzeru,Sanafuna kuopa Yehova;
30. Anakana uphungu wanga,Nanyoza kudzudzula kwanga konse;
31. Momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao,Nadzakhuta zolingalira zao.
32. Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa acibwana kudzawapha;Ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.
33. Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka,Nadzakhala phe osaopa zoipa,