22. Kodi mudzakonda zacibwana kufikira liti, acibwana inu?Onyoza ndi kukonda kunyoza,Opusa ndi kuda nzeru?
23. Tembenukani pamene ndikudzudzulani;Taonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga,Ndikudziwitsani mau anga.
24. Cifukwa ndaitana, ndipo munakana;Ndatambasula dzanja langa, ndipo panalibe analabadira;
25. Koma munapeputsa uphungu wangawonse,Ndi kukana kudzudzula kwanga.
26. Inetu ndidzacitiraciphwete tsoka lanu,Ndidzatonyola pakudza mantha anu;
27. Pakudza mantha anu ngati mphepo yopasula,Ndi pofika tsoka lanu ngati kabvumvulu;Pakudza kwa inu bvuto ndi nsautso.
28. Pamenepo adzandiitana, koma sindidzabvomera;Adzandifunatu, osandipeza ai;