Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 1:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. MIYAMBI ya Solomo mwana wa Davide, mfumu ya Israyeli.

2. Kudziwa nzeru ndi mwambo;Kuzindikira mau ozindikiritsa;

3. Kulandira mwambo wakusamalira macitidwe,Cilungamo, ciweruzo ndi zolunjika;

4. Kucenjeza acibwana,Kuphunzitsa mnyamata kudziwa ndi kulingalira;

5. Kuti wanzeru amve, naonjezere kuphunzira;Ndi kuti wozindikira afikire kuuphungu;

6. Kuzindikira mwambi ndi tanthauzo lace,Mau a anzeru, ndi zophiphiritsa zao.

7. Kuopa Yehova ndiko ciyambi ca kudziwa;Opusa anyoza nzeru ndi mwambo.

8. Mwananga, tamva mwambo wa atate wako,Ndi kusasiya cilangizo ca amako

9. Pakuti izi ndi korona wa cisomo pamtu pako,Ndi mkanda pakhosi pako.

10. Mwananga, akakukopa ocimwa usalole.

11. Akanena, Idza nafe, tibisalire mwazi,Tilalire osacimwa opanda cifukwa;

12. Tiwameze ali ndi moyo ngati manda,Ali amphumphu, ngati akutsikira kudzenje;

13. Tidzapeza cuma conse ca mtengo wace,Tidzadzaza nyumba zathu ndi zofunkha;

Werengani mutu wathunthu Miyambi 1