Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mika 3:7-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo alauli adzacita manyazi, ndi olosa adzathedwa nzeru; ndipo onsewo adzasunama; pakuti kuyankha kwa Mulungu kulibe.

8. Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi ciweruzo, ndi camuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwace, ndi kwa Israyeli cimo lace.

9. Tamvanitu ici, akuru a nyumba ya Yakobo inu, ndi oweruza a nyumba ya Israyeli inu, akuipidwa naco ciweruzo, ndi kupotoza zoongoka zonse.

10. Amanga Ziyoni ndi mwazi, ndi Yerusalemu ndi cisalungamo.

11. Akuru ace aweruza cifukwa ca mphotho, ndi ansembe ace aphunzitsa cifukwa ca malipo, ndi aneneri ace alosa cifukwa ca ndarama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? palibe coipa codzatigwera.

12. Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati: munda cifukwa ca inu, ndi m'Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.

Werengani mutu wathunthu Mika 3