Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mika 3:6-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. cifukwa cace kudzakhala ngati usiku kwa inu, wopanda masomphenya; ndipo kudzadera inu, wopanda kulosa; ndi dzuwa lidzalowera aneneri, ndi usana udzawadera bii.

7. Ndipo alauli adzacita manyazi, ndi olosa adzathedwa nzeru; ndipo onsewo adzasunama; pakuti kuyankha kwa Mulungu kulibe.

8. Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi ciweruzo, ndi camuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwace, ndi kwa Israyeli cimo lace.

9. Tamvanitu ici, akuru a nyumba ya Yakobo inu, ndi oweruza a nyumba ya Israyeli inu, akuipidwa naco ciweruzo, ndi kupotoza zoongoka zonse.

10. Amanga Ziyoni ndi mwazi, ndi Yerusalemu ndi cisalungamo.

Werengani mutu wathunthu Mika 3