Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mika 3:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ndinati, Imvanitu, inu akuru a Yakobo, ndi oweruza a nyumba ya Israyeli; simuyenera kodi kudziwa ciweruzo?

2. inu amene mudana naco cokoma ndi kukondana naco coipa; inu akumyula khungu lao pathupi pao, ndi mnofu wao pa mafupa ao;

3. inu amene mukudyanso mnofu wa anthu anga; ndi kusenda khungu lao ndi kutyola mafupa ao; inde awaduladula ngati nyama yoti aphike, ndi ngati nyama ya mumphika.

4. Pamenepo adzapfuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yace nthawi yomweyo, monga momwe anaipsa macitidwe ao.

5. Atero Yehova za aneneriakulakwitsa anthu anga; akuluma ndi mano ao, ndi kupfuula, Mtendere; ndipo, ali yense wosapereka m'kamwa mwao, amkonzera nkhondo;

6. cifukwa cace kudzakhala ngati usiku kwa inu, wopanda masomphenya; ndipo kudzadera inu, wopanda kulosa; ndi dzuwa lidzalowera aneneri, ndi usana udzawadera bii.

7. Ndipo alauli adzacita manyazi, ndi olosa adzathedwa nzeru; ndipo onsewo adzasunama; pakuti kuyankha kwa Mulungu kulibe.

Werengani mutu wathunthu Mika 3