Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 98:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Myimbireni Yehova nyimbo yatsopano;Popeza anacita zodabwiza:Dzanja lace lamanja, mkono wace woyera, zinamcitira cipulumutso,

2. Yehova anawadziwitsira cipulumutso cace;Anaonetsera cilungamo cace pamaso pa amitundu.

3. Anakumbukila cifundo cace ndi cikhulupiriko cace ku nyumba ya Israyeli;Malekezero onse a dziko lapansi anaona cipulumutso ca Mulungu wathu.

4. Pfuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi;Kuwitsani ndi kupfuulira mokondwera; inde, yimbirani zomlemekeza.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 98