Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 94:9-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Kodi Iye wakupanga khutu ngwosamva?Kodi Iye wakuumba diso ngwosapenya?

10. Kodi Iye wakulangiza mitundu ya anthu, ndiye wosadzudzula?Si ndiye amene aphunzitsa munthu nzeru?

11. Yehova adziwa zolingalira za munthu,Kuti ziri zacabe.

12. Wodala munthu amene mumlanga, Yehova;Ndi kumphunzitsa m'cilamulo canu;

13. Kuti mumpumitse masiku oipa;Kufikira atakumbira woipa mbuna.

14. Pakuti Yehova sadzasiya anthu ace,Ndipo sadzataya colandira cace.

15. Pakuti ciweruzo cidzabwera kumka kucilungamo:Ndipo oongoka mtima onse adzacitsata.

16. Adzandiukira ndani kutsutsana nao ocita zoipa?Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ocita zopanda pace?

17. Akadapanda kukhala thandizo langa Yehova,Moyo wanga ukadakhala kuli cete.

18. Pamene ndinati, Litereka phazi langa,Cifundo canu, Mulungu, cinandicirikiza.

19. Pondicurukira zolingalira zanga m'kati mwanga,Zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 94