Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 94:2-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi:Bwezerani odzikuza coyenera iwo.

3. Oipa adzatumpha ndi cimwemwe kufikira liti, Yehova?Oipa adzatero kufikira liti?

4. Anena mau, alankhula zawawa;Adzitamandira onse ocita zopanda pace.

5. Aphwanya anthu anu, Yehova,Nazunza colandira canu.

6. Amapha wamasiye ndi mlendo,Nawapha ana amasiye.

7. Ndipo amati, Yehova sacipenya,Ndi Mulungu wa Yakobo sacisamalira.

8. Zindikirani, opulukira inu mwa anthu;Ndipo opusa inu, mudzacita mwanzeru liti?

9. Kodi Iye wakupanga khutu ngwosamva?Kodi Iye wakuumba diso ngwosapenya?

10. Kodi Iye wakulangiza mitundu ya anthu, ndiye wosadzudzula?Si ndiye amene aphunzitsa munthu nzeru?

11. Yehova adziwa zolingalira za munthu,Kuti ziri zacabe.

12. Wodala munthu amene mumlanga, Yehova;Ndi kumphunzitsa m'cilamulo canu;

13. Kuti mumpumitse masiku oipa;Kufikira atakumbira woipa mbuna.

14. Pakuti Yehova sadzasiya anthu ace,Ndipo sadzataya colandira cace.

15. Pakuti ciweruzo cidzabwera kumka kucilungamo:Ndipo oongoka mtima onse adzacitsata.

16. Adzandiukira ndani kutsutsana nao ocita zoipa?Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ocita zopanda pace?

17. Akadapanda kukhala thandizo langa Yehova,Moyo wanga ukadakhala kuli cete.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 94